6 Anasanduliza nyanja ikhale mtunda:Anaoloka mtsinje coponda pansi:Apo tinakondwera mwa Iye.
7 Acita ufumu mwa mphamvu yace kosatha;Maso ace ayang'anira amitundu;Opikisana ndi Iye asadzikuze.
8 Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu,Ndipo mumveketse liu la cilemekezo cace:
9 Iye amene asunga moyo wathu tingafe,Osalola phazi lathu literereke.
10 Pakati munatiyesera, Mulungu:Munatiyenga monga ayenga siliya.
11 Munapita nafe kuukonde;Munatisenza cothodwetsa pamsana pathu.
12 Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu;Tinapyola moto ndi madzi; Koma munatifikitsa potitsitsimutsa.