2 Kuti njira yanu idziwike pa dziko lapansi,Cipulumutso canu mwa amitundu onse.
3 Anthu akuyamikeni, Mulungu;Anthu onse akuyamikeni.
4 Anthu akondwere, napfuule makondwera;Pakuti mudzaweruza anthu malunjika,Ndipo mudzalangiza anthu pa dziko lapansi.
5 Anthu akuyamikeni, Mulungu;Anthu onse akuyamikeni.
6 Dziko lapansi lapereka zipatso zace:Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.
7 Mulungu adzatidalitsa;Ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye,