27 Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwacita ufumu,Akuru a Yuda, ndi a upo wao,Akulu a Zebuloni, akulu a Naftali.
28 Mulungu wako analamulira mphamvu yako:Limbitsani, Mulungu, cimene munaticitira.
29 Cifukwa ca Kacisi wanu wa m'YerusalemuMafumu adzabwera naco caufulu kukupatsani.
30 Dzudzulani cirombo ca m'bango,Khamu la mphongo ndi zipfulula za anthu,Yense wakudzigonjera ndi ndarama zasiliva;Anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.
31 Akulu adzafumira ku Aigupto;Kushi adzafulumira kutambalitsa manja ace kwa Mulungu.
32 Yimbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu;Yimbirani Ambuye zomlemekeza;
33 Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe;Taonani; amveketsa liu lace, ndilo liu lamphamvu.