10 Cikopa canga ciri ndi Mulungu, Wopulumutsa oongoka mtima.
11 Mulungu ndiye Woweruza walungama,Ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse.
12 Akapanda kutembenuka munthu, Iye adzanola lupanga lace;Wakoka uta wace, naupiringidza.
13 Ndipo anamkonzera zida za imfa;Mibvi yace aipanga ikhale yansakali,
14 Taonani, ali m'cikuta ca zopanda pace;Anaima ndi cobvuta, nabala bodza.
15 Anacita dzenje, nalikumba,Nagwa m'mbuna yomwe anaikumba.
16 Cobvuta cace cidzambwerera mwini,Ndi ciwawa cace cidzamgwera pakati pamutu pace.