11 Ndi kuti, Wamsiya Mulungu:Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa,
12 Musandikhalire kutali, Mulungu;Fulumirani kundithandiza, Mulungu;
13 Adani a moyo wanga acite manyazi, nathawe;Cotonza ndi cimpepulo zikute ondifunira coipa,
14 Koma ine ndidzayembekeza kosaleka,Ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.
15 Pakamwa panga padzafotokozera cilungamo canu,Ndi cipulumutso canu tsiku lonse;Pakuti sindidziwa mawerengedwe ace.
16 Ndidzamuka mu mphamvu ya Ambuye Yehova;Ndidzachula cilungamo canu, inde canu cokha.
17 Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga;Ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwiza zanu.