14 Koma ine ndidzayembekeza kosaleka,Ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.
15 Pakamwa panga padzafotokozera cilungamo canu,Ndi cipulumutso canu tsiku lonse;Pakuti sindidziwa mawerengedwe ace.
16 Ndidzamuka mu mphamvu ya Ambuye Yehova;Ndidzachula cilungamo canu, inde canu cokha.
17 Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga;Ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwiza zanu.
18 Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu;Kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu,Mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.
19 Cilungamo canunso, Mulungu, cifikira kuthambo;Inu amene munacita zazikuru,Akunga Inu ndani, Mulungu?
20 Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa,Mudzatipatsanso moyo,Ndi kutitenganso munsi mwa dziko.