20 Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa,Mudzatipatsanso moyo,Ndi kutitenganso munsi mwa dziko.
21 Mundionjezere ukulu wanga,Ndipo munditembenukire kundisangalatsa,
22 Ndiponso ndidzakuyamikani ndi cisakasa,Kubukitsa coonadi canu, Mulungu wanga;Ndidzakuyimbirani Nyimbo ndi zeze,Ndinu Woyerayo wa Israyeli.
23 Milomo yanga idzapfuula mokondwera poyimbira Inu Nyimbo;Inde, moyo wanga umene munaombola.
24 Lilime langa lomwe lidzalankhula za cilungamo canu tsiku lonse:Pakuti ofuna kundicitira coipa acita manyazi, nadodoma.