1 Mulungu adziwika mwa Yuda:Dzina lace limveka mwa Israyeli.
2 Msasa wace unali m'Salemu, Ndipo pokhala Iye m'Ziyoni.
3 Pomwepo anatyola mibvi ya paota;Cikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.
4 Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka wakuposa mapiri muli acifwamba.
5 Olimba mtima cifunkhidwa cuma cao, agona tulo tao;Amuna onse amphamvu asowa manja ao.