9 Pakuuka Mulungu kuti aweruze,Kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi.
10 Indedi, kuzaza kwace kwa munthu kudzakulemekezani;Cotsalira ca kuzazaku mudzaciletsa.
11 Windani ndipo citirani Yehova Mulungu wanu zowindazo;Onse akumzinga abwere naco copereka ca kwa Iye amene ayenera kumuopa.
12 Iye adzadula mzimu wa akulu;Akhala woopsa kwa mafumu a pa dziko lapansi.