12 Ndipo ndidzalingalira nchito yanu yonse,Ndi kulingalirabe zimene munazicita Inu.
13 Mulungu, m'malo opatulika muli njira yanu;Mulungu wamkuru ndani monga Mulungu?
14 Inu ndinu Mulungu wakucita codabwiza;Munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.
15 Munaombola anthu anu ndi mkonowanu,Ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.
16 Madziwo anakuonani Mulungu;Anakuonani madziwo; anacita mantha:Zozama zomwe zinanjenjemera,
17 Makongwa anatsanula madzi;Thambo lidamvetsa liu lace;Mibvi yanu yomwe inaturukira.
18 Liu la bingu lanu linatengezanatengezana;Mphezi zinaunikira ponse pali anthu;Dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.