7 Kodi Mulungu adzataya nthawi yonse?Osabwerezanso kukondwera nafe.
8 Cifundo cace calekeka konse konse kodi?Lonjezano lace lidatha kodi ku mibadwo yonse?
9 Kodi Mulungu waiwala kucita cifundo?Watsekereza kodi nsoni zokoma zace mumkwiyo?
10 Ndipo ndinati, Cindilaka ici;Koma ndikumbukila zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba.
11 Ndidzakumbukila zimene adazicita Ambuye;Inde, ndidzakumbukila zodabwiza zanu zoyambira kale.
12 Ndipo ndidzalingalira nchito yanu yonse,Ndi kulingalirabe zimene munazicita Inu.
13 Mulungu, m'malo opatulika muli njira yanu;Mulungu wamkuru ndani monga Mulungu?