41 Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu,Nacepsa Woyerayo wa Israyeli.
42 Sanakumbukila dzanja lace,Tsikuli anawaombola kwa msautsi.
43 Amene anaika zizindikilo zace m'Aigupto,Ndi zodabwiza zace ku cidikha ca Zoanu;
44 Nasanduliza nyanja yao mwazi,Ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa.
45 Anawatumizira pakati pao mitambo ya nchenche zakuwatha;Ndi acule akuwaononga.
46 Ndipo anapatsa mphuci dzinthu dzao,Ndi dzombe nchito yao.
47 Anapha mphesa zao ndi matalala,Ndi mikuyu yao ndi cisanu.