1 Mulungu, akunja alowa m'colandira canu;Anaipsa Kacisi wanu woyera;Anacititsa Yerusalemu bwinja.
2 Anapereka mitembo ya atumiki anu ikhale cakudya ca mbalame za mlengalenga,Nyama ya okondedwa anu anaipereka kwa zirombo za m'dziko.
3 Anakhetsa mwazi wao ngati madzi pozungulira Yerusalemu;Ndipo panalibe wakuwaika.
4 Takhala cotonza ca anansi athu,Ndi coseketsa ndi colalatitsa iwo akutizinga,