2 Anapereka mitembo ya atumiki anu ikhale cakudya ca mbalame za mlengalenga,Nyama ya okondedwa anu anaipereka kwa zirombo za m'dziko.
3 Anakhetsa mwazi wao ngati madzi pozungulira Yerusalemu;Ndipo panalibe wakuwaika.
4 Takhala cotonza ca anansi athu,Ndi coseketsa ndi colalatitsa iwo akutizinga,
5 Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti?Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?
6 Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu,Ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.
7 Pakuti anathera Yakobo,Napasula pokhalira iye.
8 Musakumbukile moritsutsa mphulupulu za makolo athu;Nsoni zokoma zanu zitikumike msanga:Pakuti tafoka kwambiri.