1 Yehova, Ambuye wathu,Dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.
2 M'kamwa mwa makanda ndi oyamwamunakhazikitsamphamvu,Cifukwa ca otsutsana ndi Inu,Kuti muwaletse mdani ndi wobwezera cilango.
3 Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, nchito ya zala zanu,Mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
4 Munthu ndani kuti mumkumbukila?Ndi mwana wa munthu kuti muceza naye?