5 Pakuti munamcepsa pang'ono ndi Mulungu,Munambveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.
6 Munamcititsa ufumu pa nchito za manja anu;Mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ace;
7 Nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo,Ndi nyama za kuthengo zomwe;
8 Mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja.Zopita m'njira za m'nyanja.
9 Yehova, Ambuye wathu,Dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!