13 Ha! akadandimvera anthu anga,Akadayenda m'njira zanga Israyeli!
14 Ndikadagonjetsa adani ao msanga,Ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.
15 Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga:Koma nyengo yao ikadakhala yosatha,
16 Akadawadyetsa naye tirigu wakometsetsa:Ndikadakukhutitsanso ndi uci wa m'thanthwe.