5 Sadziwa, ndipo sazindikira;Amayendayenda mumdima;Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
6 Ndinati Ine, Inu ndinu milungu,Ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu.
7 Komatu mudzafa monga anthu,Ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.
8 Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi;Pakuti Inu mudzalandira amitundu onse.