11 Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu;Mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna:
12 Amene anati, TilandeMalo okhalamo Mulungu, akhale athu.
13 Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu;Ngati ziputu zomka ndi mphepo.
14 Monga moto upsereza nkhalango,Ndi monga lawi liyatsa mapiri;
15 Momwemo muwatsate ndi namondwe,Nimuwaopse ndi kabvumvulu wanu.
16 Acititseni manyazi pankhope pao;Kuti afune dzina lanu, Yehova.
17 Acite manyazi, naopsedwe kosatha;Ndipo asokonezeke, naonongeke: