15 Momwemo muwatsate ndi namondwe,Nimuwaopse ndi kabvumvulu wanu.
16 Acititseni manyazi pankhope pao;Kuti afune dzina lanu, Yehova.
17 Acite manyazi, naopsedwe kosatha;Ndipo asokonezeke, naonongeke:
18 Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,Ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.