4 Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu;Ndipo dzina la Israyeli lisakumbukikenso.
5 Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi;Anacita cipangano ca pa Inu:
6 Mahema a Edomu ndi a Aismayeli;Moabu ndi Ahagara;
7 Gebala ndi Amoni ndi Amaleki;Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala m'Turo.
8 Asuri anaphatikana nao;Anakhala dzanja la ana a Loti,
9 Muwacitire monga munacitira Midyani;Ndi Sisera, ndi Jabini ku mtsinje wa Kisoni:
10 Amene anaonongeka ku Endoro;Anakhala ngati ndowe ya kumunda.