3 Mbawanso inapeza nyumba,Ndi namzeze cisa cace coikamo ana ace,Pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu,Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,
4 Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu;Akulemekezani cilemekezere,
5 Wodala munthu amene mphamvu yace iri mwa Inu;Mumtima mwace muli makwalala a ku Ziyoni,
6 Popyola cigwa ca kulira misozi aciyesa ca akasupe;Inde mvula: ya cizimalupsa icidzaza ndi madalitso.
7 Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu,Aoneka pamaso pa Mulungu m'Ziyoni.
8 Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa:Cherani khutu, Mulungu wa Yakobo.
9 Onani, Mulungu, ndinu cikopa cathu;Ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.