8 Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa:Cherani khutu, Mulungu wa Yakobo.
9 Onani, Mulungu, ndinu cikopa cathu;Ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.
10 Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena,Kukhala inewapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga,Kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a coipa,
11 Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi cikopa;Yehova adzapatsa cifundo ndi ulemerero;Sadzakaniza cokoma iwo akuyenda angwiro,
12 Yehova wa makamu,Wodala munthu wakukhulupirira Inu.