1 Munacita zobvomereza dziko lanu, Yehova;Munabweza ukapolo wa Yakobo.
2 Munacotsa mphulupulu ya anthu anu,Munafotsera zolakwa zao zonse.
3 Munabweza kuzaza kwanu konse;Munabwerera ku mkwiyo wanu wotentha.
4 Mutibweze, Mulungu wa cipulumutso cathu,Nimuletse udani wanu wa pa ife.