1 Munacita zobvomereza dziko lanu, Yehova;Munabweza ukapolo wa Yakobo.
2 Munacotsa mphulupulu ya anthu anu,Munafotsera zolakwa zao zonse.
3 Munabweza kuzaza kwanu konse;Munabwerera ku mkwiyo wanu wotentha.
4 Mutibweze, Mulungu wa cipulumutso cathu,Nimuletse udani wanu wa pa ife.
5 Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?Kodi mudzakhala cikwiyire mibadwo mibadwo?
6 Kodi simudzatipatsanso moyo,Kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?
7 Tionetseni cifundo canu, Yehova,Tipatseni cipulumutso canu.