1 Yehova, Mulungu wa cipulumutso canga,Ndinapfuula pamaso panu usana ndi usiku,
2 Pemphero langa lidze pamaso panu;Mundicherere khutu kukuwa kwanga:
3 Pakuti mzimu wanga wadzala nao mabvuto,Ndi moyo wanga wayandikira kumanda.
4 Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje;Ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu: