12 Zodabwiza zanu zidzadziwika mumdima kodi,Ndi cilungamo canu m'dziko la ciiwaliko?
13 Koma ndinapfuulira kwa Inu, Yehova,Ndipo pemphero langa likumika Inu mamawa.
14 Yehova mutayiranji moyo wanga?Ndi kundibisira nkhope yanu?
15 Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga;Posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.
16 Kuzaza kwanu kwandimiza;Zoopsa zanu zinandiononga,
17 Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse;Zinandizinga pamodzi.
18 Munandicotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa,Odziwana nane akhala kumdima.