2 Pemphero langa lidze pamaso panu;Mundicherere khutu kukuwa kwanga:
3 Pakuti mzimu wanga wadzala nao mabvuto,Ndi moyo wanga wayandikira kumanda.
4 Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje;Ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu:
5 Wotayika pakati pa akufa,Ngati ophedwa akugona m'manda,Amene simuwakumbukilanso;Ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.
6 Munandiika kunsi kwa dzenje,Kuti mdima, kozama.
7 Mkwiyo wanu utsamira pa ine,Ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.
8 Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;Munandiika ndiwakhalire conyansa:Ananditsekereza osakhoza kuturuka ine.