8 Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;Munandiika ndiwakhalire conyansa:Ananditsekereza osakhoza kuturuka ine.
9 Diso langa lapuwala cifukwa ca kuzunzika kwanga:Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse;Nditambalitsira manja anga kwa Inu.
10 Kodi mudzacitira akufa zodabwiza?Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani?
11 Adzafotokozera cifundo canu kumanda kodi,Cikhulupiriko canu ku malo a cionongeko?
12 Zodabwiza zanu zidzadziwika mumdima kodi,Ndi cilungamo canu m'dziko la ciiwaliko?
13 Koma ndinapfuulira kwa Inu, Yehova,Ndipo pemphero langa likumika Inu mamawa.
14 Yehova mutayiranji moyo wanga?Ndi kundibisira nkhope yanu?