1 Ndidzayimbira zacifundo za Yehova nthawi yonse:Pakamwa panga ndidzadziwitsira cikhulupiriko canu ku mibadwo mibadwo.
2 Pakuti ndinati, Cifundo adzacimanga kosaleka;Mudzakhazika cikhulupiriko canu m'Mwamba mweni mweni.
3 Ndinacita cipangano ndi wosankhika wanga,Ndinalumbirira Davide mtumiki wanga:
4 Ndidzakhazika mbeu yako ku nthawi yonse,Ndipo ndidzamanga mpando wacifumu wako ku mibadwo mibadwo.