12 Munalenga kumpoto ndi kumwela;Tabora ndi Hermoni apfuula mokondwera m'dzina lanu.
13 Muli nao mkono wanu wolimba;M'dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka.
14 Cilungamo ndi ciweruzo ndiwo maziko a mpando wacifumu wanu;Cifundo ndi coonadi zitsogolera pankhope panu.
15 Odala anthu odziwa liu la lipenga;Ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
16 Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse;Ndipo akwezeka m'cilungamo canu.
17 Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao;Ndipo potibvomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.
18 Pakuti cikopa cathu cifuma kwa Yehova;Ndi mfumuyathu kwa Woyera wa Israyeli.