29 Ndidzakhalitsanso mbeu yace cikhalire,Ndi mpando wacifumu wace ngati masiku a m'mwamba.
30 Ana ace akataya cilamulo canga,Osayenda m'maweruzo anga:
31 Nakaipsa malembo anga;Osasunga malamulo anga;
32 Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo,Ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.
33 Koma sindidzamcotsera cifundo canga conse,Ndi cikhulupiriko canga sicidzamsowa.
34 Sindidzaipsa cipangano canga,Kapena kusintha mau oturuka m'milomo yanga.
35 Ndinalumbira kamodzi m'ciyero canga;Sindidzanamizira Davide;