36 Mbeu yace idzakhala ku nthawi yonse,Ndi mpando wacifumu wace ngati dzuwa pamaso panga.
37 Udzakhazikika ngati mwezi ku nthawi yonse,Ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.
38 Koma Inu munamtaya, nimunamkaniza,Munakwiya naye wodzozedwa wanu.
39 Munakaniza cipangano ca mtumiki wanu;Munaipsa korona wace ndi kumponya pansi,
40 Munapasula maguta ace onse;Munagumula malinga ace.
41 Onse opita panjirapa amfunkhira:Akhala cotonza ca anansi ace.
42 Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa;Munakondweretsa adani ace onse.