37 Udzakhazikika ngati mwezi ku nthawi yonse,Ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.
38 Koma Inu munamtaya, nimunamkaniza,Munakwiya naye wodzozedwa wanu.
39 Munakaniza cipangano ca mtumiki wanu;Munaipsa korona wace ndi kumponya pansi,
40 Munapasula maguta ace onse;Munagumula malinga ace.
41 Onse opita panjirapa amfunkhira:Akhala cotonza ca anansi ace.
42 Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa;Munakondweretsa adani ace onse.
43 Munapinditsa kukamwa kwace kwa lupanga lace,Osamuimika kunkhondo.