4 Ndidzakhazika mbeu yako ku nthawi yonse,Ndipo ndidzamanga mpando wacifumu wako ku mibadwo mibadwo.
5 Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwiza zanu, Yehova;Cikhulupiriko canunso mu msonkhano wa oyera mtima.
6 Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova?Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?
7 Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri m'upo wa oyera mtima,Ndiye wocititsa mantha koposa onse akumzinga.
8 Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova?Ndipo cikhulupiriko canu cikuzingani.
9 Inu ndinu wakucita ufumu pa kudzikuza kwa nyanja;Pakuuka mafunde ace muwacititsa bata.
10 Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa;Munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.