42 Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa;Munakondweretsa adani ace onse.
43 Munapinditsa kukamwa kwace kwa lupanga lace,Osamuimika kunkhondo.
44 Munaleketsa kuwala kwace,Ndipo munagwetsa pansi mpando wacifumu wace.
45 Munafupikitsa masiku a mnyamata wace;Munamkuta nao manyazi.
46 Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova;Ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?
47 Kumbukilani kuti nthawi yanga njapafupi;Munalengeranji ana onse a anthu kwacabe?
48 Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa?Amene adzapulumutsa moyo wace ku mphamvu ya manda?