45 Munafupikitsa masiku a mnyamata wace;Munamkuta nao manyazi.
46 Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova;Ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?
47 Kumbukilani kuti nthawi yanga njapafupi;Munalengeranji ana onse a anthu kwacabe?
48 Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa?Amene adzapulumutsa moyo wace ku mphamvu ya manda?
49 Ciri kuti cifundo canu cakale, Ambuye,Munacilumbirira Davide pa cikhulupiriko canu?
50 Kumbukilani, Ambuye, cotonzera atumiki anu;Ndicisenza m'cifuwa mwanga cacokera ku mitundu yonse yaikuru ya anthu;
51 Cimene adani anu, Yehova, atonza naco;Cimene atonzera naco mayendedwe a wodzozedwa wanu.