49 Ciri kuti cifundo canu cakale, Ambuye,Munacilumbirira Davide pa cikhulupiriko canu?
50 Kumbukilani, Ambuye, cotonzera atumiki anu;Ndicisenza m'cifuwa mwanga cacokera ku mitundu yonse yaikuru ya anthu;
51 Cimene adani anu, Yehova, atonza naco;Cimene atonzera naco mayendedwe a wodzozedwa wanu.
52 Wodalitsika Yehova ku nthawi yonse,Amen ndi Amen.