6 Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova?Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?
7 Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri m'upo wa oyera mtima,Ndiye wocititsa mantha koposa onse akumzinga.
8 Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova?Ndipo cikhulupiriko canu cikuzingani.
9 Inu ndinu wakucita ufumu pa kudzikuza kwa nyanja;Pakuuka mafunde ace muwacititsa bata.
10 Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa;Munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.
11 Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu;Munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwace.
12 Munalenga kumpoto ndi kumwela;Tabora ndi Hermoni apfuula mokondwera m'dzina lanu.