2 Asanabadwe mapiri,Kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu,Inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha,Inu ndinu Mulungu.
3 Mubweza munthu akhale pfumbi;Nimuti, Bwererani inu, ana a anthu.
4 Pakuti pamaso panu zaka zikwiZikhala ngati dzulo, litapita,Ndi monga ulonda wa usiku.
5 Muwatenga ngati ndi madzi akulu, akhala ngati tulo;Mamawa akhala ngati msipu waphuka.
6 Mamawa uphuka bwino;Madzulo ausenga, nuuma.
7 Pakuti tionongeka mu mkwiyo wanu;Ndipo m'kuzaza kwanu tiopsedwa.
8 Munaika mphulupulu zathu pamaso panu,Ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.