1 Iye amene akhala pansi m'ngaka yace ya Wam'mwambamwambaAdzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
2 Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa;Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira,
3 Pakuti adzakuonjola ku msampha wa msodzi,Ku mliri wosakaza.
4 Adzakufungatira ndi nthenga zace,Ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ace;Coonadi cace ndico cikopa cocinjiriza.