4 Adzakufungatira ndi nthenga zace,Ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ace;Coonadi cace ndico cikopa cocinjiriza.
5 Sudzaopa coopsa ca usiku, Kapena mubvi wopita usana;
6 Kapena mliri woyenda mumdima,Kapena cionongeko cakuthera usana.
7 Pambali pako padzagwa cikwi,Ndi zikwi khumi pa dzanja lamanja lako;Sicidzakuyandikiza iwe.
8 Koma udzapenya ndi maso ako,Nudzaona kubwezera cilango oipa.
9 Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo pangaUdaika Wam'mwambamwamba cokhalamo cako;
10 Palibe coipa cidzakugwera,Ndipo colanga sicidzayandikiza hema wako.