8 Koma udzapenya ndi maso ako,Nudzaona kubwezera cilango oipa.
9 Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo pangaUdaika Wam'mwambamwamba cokhalamo cako;
10 Palibe coipa cidzakugwera,Ndipo colanga sicidzayandikiza hema wako.
11 Pakuti adzalamulira angelo ace za iwe,Akusunge m'njira zako zonse.
12 Adzakunyamula pa manja ao,Ungagunde phazi lako pamwala.
13 Udzaponda mkango ndi mphiri;Udzapondereza msona wa mkango ndi cinjoka:
14 Popeza andikondadi ndidzampulumutsa;Ndidzamkweza m'mwamba, papeza adziwa dzina langa.