1 Nkokoma kuyamika Yehova,Ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu:
2 Kuonetsera cifundo canu mamawa,Ndi cikhulupiriko canu usiku uli wonse.
3 Pa coyimbira ca zingwe khumi ndi pacisakasa;Pazeze ndi kulira kwace.
4 Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kucita kwanu,Ndidzapfuula mokondwera pa nchito ya manja anu.
5 Ha! nchito zanu nzazikuru, Yehova,Zolingalira zanu nzozama ndithu.