12 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;Adzakula ngati mkungudza wa ku Lebano.
13 Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova,Adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.
14 Atakalamba adzapatsanso zipatso;Adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri:
15 Kulalikira kuti Yehova ngwolunjika;Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe cosalungama.