2 Kuonetsera cifundo canu mamawa,Ndi cikhulupiriko canu usiku uli wonse.
3 Pa coyimbira ca zingwe khumi ndi pacisakasa;Pazeze ndi kulira kwace.
4 Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kucita kwanu,Ndidzapfuula mokondwera pa nchito ya manja anu.
5 Ha! nchito zanu nzazikuru, Yehova,Zolingalira zanu nzozama ndithu.
6 Munthu wopulukira sacidziwa;Ndi munthu wopusa sacizindikira ici;
7 Cakuti pophuka oipa ngati msipu,Ndi popindula ocita zopanda pace;Citero kuti adzaonongeke kosatha:
8 Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba ku nthawi yonse.