6 Munthu wopulukira sacidziwa;Ndi munthu wopusa sacizindikira ici;
7 Cakuti pophuka oipa ngati msipu,Ndi popindula ocita zopanda pace;Citero kuti adzaonongeke kosatha:
8 Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba ku nthawi yonse.
9 Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,Pakuti, taonani, adani anu adzatayika;Ocita zopanda pace onse adzamwazika.
10 Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati;Anandidzoza mafuta atsopano.
11 Diso langa lapenya cokhumba ine pa iwo ondilalira,M'makutu mwanga ndamva cokhumba ine pa iwo akucita zoipa akundiukira.
12 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;Adzakula ngati mkungudza wa ku Lebano.