1 Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano;Myimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.
2 Myimbireni Yehova, lemekezani dzina lace;Lalikirani cipulumutso cace tsiku ndi tsiku.
3 Fotokozerani ulemerero wace mwa amitundu;Zodabwiza zace mwa mitundu yonse ya anthu.
4 Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;Ayenera amuope koposa milungu yonse.
5 Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano:Koma Yehova analenga zakumwamba.