5 Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano:Koma Yehova analenga zakumwamba.
6 Pamaso pace pali ulemu ndi ukulu:M'malo opatulika mwace muli mphamvu ndi zocititsa kaso.
7 Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu,Mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu,
8 Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lace;Bwerani naco copereka, ndipo fikani ku mabwalo ace.
9 Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa:Njenjemerani pamaso pace, inu dziko lonse lapansi.
10 Nenani mwa amitundu, Yehova acita ufumu;Dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke;Adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
11 Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi;Nyanja ibume mwa kudzala kwace: