4 Mphezi zace zinaunikira dziko lokhalamo anthu;Dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.
5 Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,Pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
6 Kumwamba kulalikira cilungamo cace,Ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wace.
7 Onse akutumikira fano losema,Akudzitamandira nao mafano, acite manyazi:Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.
8 Ziyoni anamva nakondwera,Nasekerera ana akazi a Yuda;Cifukwa ca maweruzo anu, Yehova.
9 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,Ndinu wokwezeka kwakukuru pamwamba pa milungu yonse yina.
10 Inuokonda Yehova, danani naco coipa:Iye asunga moyo wa okondedwa ace;Awalanditsa m'manja mwa oipa.